1. Ndipo ine, abale, sindinakhoza kulankhula ndi inu manga ndi auzimu, koma monga athupi, monga makanda mwa Kristu.
2. Ndinaiyetsa inu mkaka, si cakudya colimba ai; pakuti simunaeikhoza; ngakhale tsopano lino simucikhoza; pakuti mulinso athupi;
3. pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndeu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu?
4. Pakuti pamene wina anena, ine ndine wa Paulo; koma mnzace, Ndine wa Apolo; simuli anthu kodi?
5. Ndipo Apolo nciani, ndi Paulo nciani? Atumiki amene munakhulupirira mwa iwo, yense monga Ambuye anampatsa.
6. Ndinanka ine, anathirira Apolo; kama Mulungu anakulitsa.
7. Cotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; kama Mulungu amene akulitsa.