1. Koma za copereka ca kwa oyera mtima, mongandinalangiza Mipingo ya ku Galatiya, motero citani inunso.
2. Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha; monga momwe anapindula, kuti zopereka zisacitike pakudza ine.
3. Ndipo pamene ndifika, ndidzatuma iwo amene mudzawayesa oyenera, ndi akalata, apite nayo mphatso yanu ku Yerusalemu.