12. Koma ngati Kristu alalikidwa kuti waukitsidwa kwa akufa, nanga ena mwa inu anena bwanjikuti kulibe kuuka kwa akufa?
13. Koma ngati kulibe kuuka kwa akufa, Kristunso sanaukitsidwa;
14. ndipo ngati Kristu sanaukitsidwakulalikira kwathu kuli cabe, cikhulupiriro canunso ciri cabe.
15. Ndiponso ife tipezedwa mboni zonama za Mulungu; cifukwa n tinacita umboni kunena za Mulungu kuti anaukitsa Kristu; amene sanamuukitsa, ngati kuli tero kuti akufa saukitsidwa,
16. Pakuti ngati akufa saukitsidwa, Kristunso sanaukitsidwa;
17. ndipo ngati Kristu sanaukitsidwa, cikhulupiriro canu ciri copanda pace; muli cikhalire m'macimo anu.
18. Cifukwa cace iwonso akugona mwa Kristu anatayika.
19. Ngati tiyembekezera Kristu m'moyo uno wokha, tiri ife aumphawi oposa a anthu onse,
20. Koma tsopano Kristu waukitsidwa kwa akufa, cipatso coundukula ca iwo akugona.
21. Pakuti monga imfa inadza mwa munthu, kuuka kwa akufa kunadzanso mwa munthu.