1. Ndipo ndikudziwitsani, abale, Uthenga Wabwino umene ndinakulalikirani inu, umenenso munalandira, umenenso muimamo,
2. umenenso mupulumutsidwa nao ngati muugwiritsa monga momwe ndinalalikira kwa inu; ngati simunakhulupira cabe.
3. Pakuti ndinapereka kwa inu poyamba, cimenenso ndinalandira, kuti Kristuanafera zoipa zathu, mongamwa malembo;
4. ndi kuti anaikidwa; ndi kutianaukitsidwa tsiku lacitatu, monga mwa malembo;
5. ndi kuti anaonekera kwa Kefa; pamenepo kwa khumi ndi awiriwo;