12. Pakuti monga mkazi aliwa kwa mwamuna, comweconso mwamuna ali mwa mkazi; koma zinthu zonse ziri za kwa Mu, lungu.
13. Lingirirani mwa inu nokha: Kodi nkuyenera kuti apemphere kwa Mulungu, wosapfunda mutu?
14. Kodi ubadwidwe womwe sutiphunzitsa kuti ngati mwamuna aweta tsitsi cimnyozetsa iye?
15. Koma ngati mkazi aweta tsitsi, kuli ulemerero kwa iye; pakuti tsitsi lace lapatsidwa kwa iye ngati cophimba.