7. Si ndiwo mau Yehova anawalalikira mwa aneneri oyamba aja, muja Yerusalemu anali nao okhalamo, ndi wokhazikika; ndi m'midzi mwace pozungulira pace, ndi m'dziko la kumwela, ndi m'cidikha munali anthu okhalamo?
8. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Zekariya, ndi kuti,
9. Watero Yehova wa makamu, kuti, Weruzani ciweruzo coona, nimucitire yense mnzace cifundo ndi ukoma mtima;
10. musazunza mkazi wamasiye, kapena ana amasiye, mlendo kapena waumphawi; ndipo nnena mmodzi wa inu alingirire m'mtima mwace kumcitira coipa munthu mnzace.