Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Tambasula nthungo iri m'dzanja lako iloze ku Ai, pakuti ndidzaupereka m'dzanja lako. Ndipo Yoswa anatambasula nthungoyo inali m'dzanja lace kuloza mudzi.