Pamenepo anyamata ozondawo analowa, naturutsa Rahabi, ndi atate wace ndi mai wace ndi abale ace, ndi onse anali nao; anaturutsanso acibale ace onse; nawaika kunja kwa cigono ca Israyeli.