Pakuti ana a Yosefe ndiwo mapfuko awiri, Manase ndi Efraimu; ndipo sanawagawira Alevi kanthu m'dziko, koma midzi yokhalamo ndi dziko lozungulirako likhale la zoweta zao ndi cuma cao.