9. Wolenga Mlalang'amba, Akamwiniatsatana, ndi Nsangwe,Ndi Kumpotosimpita,
10. Wocita zazikuru zosasanthulika,Ndi zodabwiza zosawerengeka,
11. Taona, Mulungu apita pali ine, koma sindimpenya;Napitirira, koma osamaindikira ine.
12. Taona, akwatula, adzambwezetsa ndani?Adzanena naye ndani, Mulikucita ciani?
13. Mulungu sadzabweza mkwiyo wace;Athandizi odzikuza awerama pansi pa Iye.
14. Nanga ine tsono ndidzamyankha bwanji,Ndi kusankha mau anga akutsutsana ndi Iye?
15. Ameneyo, cinkana ndikadakhala wolungama, sindikadamyankha; Ndikadangompembedza wondiweruza ine.
16. Ndikadaitana, ndipo akadayankha Iye,Koma sindikadakhulupirira kuti Iye wamvera mau anga,
17. Pakuti andityola ndi mkuntho,Nacurukitsa mabala anga kopanda cifukwa.
18. Sandilola kuti ndipume,Koma andidzaza ndi zowawa.