8. Diso la amene andiona silidzandionanso,Maso ako adzandipenyetsetsa, koma ine palibe.
9. Mtambo wapita watha,Momwemo wakutsikira kumanda sadzakwerakonso.
10. Sadzabweranso ku nyumba yace,Osamdziwanso malo ace.
11. Potero sindidzaletsa pakamwa panga;Ndidzalankhula popsinjika mumzimu mwanga;Ndidzadandaula pakuwawa mtima wanga.
12. Ndine nyanja kodi, kapena cinjoka ca m'nyanja,Kuti Inu mundiikira odikira?
13. Ndikati, Pakama panga mpondisangalatsa,Pogona panga padzacepsa condidandaulitsa;
14. Pamenepo mundiopsa ndi maloto,Nimundicititsa mantha ndi masomphenya;
15. Potero moyo wanga usankha kupotedwa,Ndi imfa, koposa mafupa anga awa.
16. Ndinyansidwa nao moyo wanga; sindidzakhala ndi moyo cikhalire;Mundileke; pakuti masiku anga ndi acabe.
17. Munthu ndani kuti mumkuze,Ndi kuti muike mtima wanu pa iye,
18. Ndi kuti muceze naye m'mawa ndi m'mawa,Ndi kumuyesa nthawi zonse?