1. Kodi munthu alibe nkhondo kunja kuno?Kodi masiku ace sakunga masiku a wolembedwa nchito?
2. Monga kapolo woliralira mthunzi,Monga wolembedwa nchito ayembekezera mphotho yace,
3. Momwemo anandilowetsa miyezi yopanda pace.Nandiikiratu zowawa usiku ndi usiku.
4. Ndigona pansi, ndikuti,Ndidzauka liti? koma usiku undikulira;Ndipo ndimapalapata mpaka mbanda kuca.
5. Mnofu wanga wabvala mphutsi ndi nkanambo zadothi;Khungu langa lang'ambika, nilinyansa.