10. Pamenepo ndidzasangalala,Ndidzakondwera naco cowawa cosandileka;Pakuti sindinawabisa mau a Woyerayo.
11. Mphamvu yanga njotani kuti ndiyembekeze?Mathedwe anga ndi otani kuti ndipirire?
12. Kodi mphamvu yanga ndiyo mphamvu ya miyala?Mnofu wanga ndi mkuwa kodi?
13. Mulibe thandizo mwa ine ndekha; cipulumutso candithawa.
14. Iye amene akadakomoka, bwenzi lace ayenera kumcitira cifundo;Angaleke kuopa Wamphamvuyonse.
15. Abale anga anacita monyenga ngati kamtsinje,Ngati madzi a timitsinje akupitirira.
16. Amada cifukwa ca madzi oundana.M'menemo cipale cofewa cibisika;
17. Atafikira mafundi, mitsinje iuma;Kukatentha, imwerera m'malo mwao.
18. Aulendo akutsata njira yao apambukapo,Akwerera poti se, natayika.
19. Aulendo a ku Tema anapenyerera,Makamu a ku Seba anaiyembekezera.
20. Anazimidwa popeza adaikhulupirira;Anafikako, nathedwa nzeru.
21. Pakuti tsopano mukhala mamwemo;Muona coopsa, mucitapo mantha.
22. Ngati ndinati, Mundipatse?Kapena, Muperekeko kwa ine cuma canu?
23. Kapena, Mundilanditse m'dzanja la mdani?Kapena, Mundiombole m'dzanja la oopsa?