3. Pamenepo Yobu anayankha Yehova, nati,
4. Taonani, ndakhululuka ine, ndidzakubwezerani mau otani?Ndigwira pakamwa.
5. Ndalankhula kamodzi, koma sindidzayankha;Inde kawiri, koma sindionjezanso.
6. Ndipo Yehova anamyankha Yobu m'kabvumvulu, nati,
7. Dzimangire m'cuuno tsono ngati mwamuna;Ndidzakufunsa, undidziwitse.
8. Cingakhale ciweruzo canga udzacityola kodi?Udzanditsutsa kuti ndiri woipa kodi, kuti ukhale wolungama ndiwe?
9. Kodi uli nalo dzanja ngati Ine Mulungu?Kapena ukhoza kugunda ndi mau ngati Ine?