1. Ndipo Elihu anabwereza kunena, nati,
2. Tamverani mau anga, inu anzeru;Mundicherere khutu inu akudziwa.
3. Pakuti khutu liyesa mau,Monga m'kamwa mulawa cakudya.
4. Tidzisankhire coyeneraco,Tidziwe mwa tokha cokomaco.
5. Pakuti Yobu wanena, Ine ndine wolungama,Ndipo Mulungu wandicotsera coyenera ine.