21. Mnofu wace udatha, kuti sungapenyeke;Ndi mafupa ace akusaoneka aturuka.
22. Inde wasendera kufupi ku manda,Ndi moyo wace kwa akuononga.
23. Akakhala kwa iye mthenga,Womasulira mau mmodzi mwa cikwi,Kuonetsera munthu comuyenera;
24. Pamenepo Mulungu amcitira cifundo, nati,Mlanditse, angatsikire kumanda,Ndampezera dipo.
25. Mnofu wace udzakhala se, woposa wa mwana;Adzabwerera ku masiku a ubwana wace.