12. Anandilandiriranji maondo?Kapena mabere kuti ndiyamwe?
13. Pakuti ndikadagona pansi pomwepo ndi kukhala cete;Ndikanagona tulo; pamenepo ndikadaona popumula;
14. Pamodzi ndi mafumu ndi maphungu a padziko,Akudzimangira m'mabwinja;
15. Kapena pamodzi ndi akalonga eni ace a golidi,Odzaza nyumba zao ndi siliva;
16. Kapena ngati nsenye yobisika ndikadakhala kuli zi;Ngati makanda osaona kuunika.
17. Apo oipa aleka kumabvuta;Ndi apo ofoka mphamvu akhala m'kupumula.
18. Apo a m'kaidi apumula pamodzi,Osamva mau a wofulumiza wao.
19. Ang'ono ndi akulu ali komwe;Ndi kapolo amasuka kwa mbuyace.
20. Amninkhiranji kuunika wobvutika,Ndi moyo kwa iye wakuwawa mtima,