1. Atatero, Yobu anatsegula pakamwa pace, natemberera tsiku lace.
2. Nalankhula Yobu nati,
3. Litayike tsiku lobadwa ine,Ndi usikuwo udati, Waima naye mwana wamwamuna.
4. Tsiku lija likhale mdima;Mulungu asalifunse kumwamba,Ndi kuunika kusaliwalire.
5. Mdima ndi mthunzi wa imfa ziliyese lao lao;Mtambo ulikhalire;Zonse zodetsa usana bi ziliopse.
6. Usiku uja, mdima weni weni uugwere;Usakondwerere mwa masiku a m'caka;Usalowe m'ciwerengedwe ca miyezi.
7. Ha! usiku uja ukhale cumba;Kuyimbira kokondwera kusalowem'mwemo.
8. Autemberere iwo akutemberera usana,Odziwa kuutsa cinjokaco.
9. Nyenyezi za cizirezire zide;Uyembekezere kuunika, koma kuusowe;Usaone kuphenyuka kwa mbanda kuca;
10. Popeza sunatseka pa makomo ace mimba ya mai wanga.Kapena kundibisira mabvuto pamaso panga.
11. Ndinalekeranji kufera m'mimba?Ndi kupereka mzimu wanga pobadwa ine?