21. Popeza pabisikira maso a zamoyo zonse,Pabisikiranso mbalame za m'mlengalenga,
22. Cionongeko ndi Imfa zikuti,Tamva mbiri yace m'makutu mwathu.
23. Mulungu ndiye: azindikira njira yace,Ndiye adziwa pokhala pace.
24. Pakuti apenyerera malekezero a dziko lapansi,Naona pansi pa thambo ponse;
25. Pamene anaikira mphepo muyeso wace,Nayesera madzi miyeso;
26. Pakucitira mvula lamulo,Ndi njira yoyendamo mphezi ya bingu;
27. Pamenepo anaiona nzeru, naifotokozera;Anaikonza, naisanthula.
28. Koma kwa munthu anati,Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru;Ndi kupatukana naco coipa ndiko luntha.