4. Ndipo ngati ndalakwa ndithu,Kulakwa kwanga kuli ndi ine ndekha.
5. Ngati inu mudzikuza ndithu pa ine,Ndi kundichulira mtonzo wanga kuti munditsutse nao;
6. Dziwani tsopano kuti Mulungu wandikhotetsera mlandu wanga,Nandizinga ndi ukonde wace.
7. Taonani, ndipfuula kuti, Ciwawa! koma sandimvera;Ndikuwa, koma palibe ciweruzo.
8. Iye ananditsekera njira kuti ndisapitireko,Naika mdima poyendapo ine.
9. Anandibvula ulemerero wanga,Nandicotsera korona pamutu panga,
10. Nandigamula ponsepo, ndipo ndamukatu;Nacizula ciyembekezo canga ngati mtengo.
11. Wandiyatsiranso mkwiyo wace,Nandiyesera ngati wina wa adani ace.
12. Ankhondo ace andidzera pamodzi, nandiundira njira yao,Nandimangira misasa pozinga hema wanga.