1. Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha, nati,
2. Musaka mau kufikira liti?Zindikirani, ndi pamenepo tidzanena.
3. Tiyesedwa bwanji ngati nyama za kuthengo,Ndi kukhala odetsedwa pamaso panu?
4. Iwe wodzing'amba mumkwiyo mwako,Kodi dziko lapansi lisiyidwe cifukwa ca iwe?Kapena thanthwe lisunthike m'malo mwace?
5. Inde, kuunika kwa woipa kudzazima,Ndi lawi la moto wace silidzawala.