22. Sakhulupirira kuti adzaturukamo mumdima,Koma kuti lupanga limlindira;
23. Ayendayenda ndi kufuna cakudya, nati, Ciri kuti?Adziwa kuti lamkonzekeratu pafupi tsiku lamdima,
24. Nsautso ndi cipsinjo zimcititsa mantha,Zimlaka ngati mfumu yokonzekeratu kunkhondo;
25. Pakuti amtambasula dzanja lace moyambana ndi Mulungu,Napikisana ndi Wamphamvuyonse.
26. Amthamangira Iye mwaliuma,Ndi zikopa zace zocindikira.
27. Popeza anakuta nkhope yace ndi kunenepa kwace,Nacita mafunyenye a mafuta m'zuuno zace;
28. Adzakhala m'midzi yopasuka,M'nyumba zosakhalamo munthu,Zoti zisandulika muunda.
29. Sadzakhala wolemera, ndi cuma cace sicidzakhalitsa,Ndi zipatso zace sizidzacuruka padziko.
30. Sadzacoka mumdima;Lawi la moto lidzaumitsa nthambi zace;Ndipo adzacoka ndi mpumo wa m'kamwa mwace.