1. Pamenepo Yobu anayankha, nati,
2. Zoonadi inu ndinu anthu,Ndi nzeru idzafa pamodzi ndi inu.
3. Koma inenso ndiri nayo nzeru monga inu.Sindingakucepereni;Ndani sadziwa zonga izi?
4. Ndine ngati munthu wosekedwa ndi mnansi wace,Ndinaitana kwa Mulungu, ndipo anandiyankha;Munthu wolungama wangwiro asekedwa.
5. Munthu wosatekeseka apeputsa tsoka mumtima mwace,Limlindira woterereka mapazi ace.
6. Mahema a acifwamba akhala mumtendere,Ndi iwo oputa Mulungu alimbika mtima:Amene Mulungu amadzazira dzanja lao.
7. Tafunsira tsono kwa nyamazo, zidzakulangiza,Ndi mbalame za m'mlengalenga, zidzakuuza;
8. Kapena ulankhule ndi dziko lapansi, lidzakulangiza;Ndi nsomba za kunyanja, zidzakufotokozera,
9. Ndaniyo sadziwa nazo izi zonse;Kuti dzanja la Yehova licita ici?
10. M'dzanja mwace muli mpweya wa zamoyo zonse,Ndi mzimu wa munthu ali yense.