14. Mukakhala mphulupulu m'dzanja lako, uicotseretu kutali,Ndi cisalungamo cisakhale m'mahema mwako;
15. Popeza pamenepo udzakweza nkhope yako opanda banga;Nudzalimbika osacita mantha;
16. Pakuti udzaiwala cisoni cako,Udzacikumbukila ngati madzi opita;
17. Ndipo moyo wako udzayera koposa usana;Kungakhale kuli mdima kudzakhala ngati m'mawa.
18. Ndipo udzalimbika mtima popeza pali ciyembekezo;Nudzafunafuna, ndi kugona mosatekeseka,
19. Inde udzagona pansi, wopanda wina wakukunjenjemeretsa,Ndipo ambiri adzakupembedza,
20. Koma maso a oipa adzagoma, Ndi pothawirapo padzawasowa,Ndipo ciyembekezo cao ndico kupereka mzimu wao.