1. Mtima wanga ulema nao moyo wanga,Ndidzadzilolera kudandaula kwanga,Ndidzalankhula pakuwawa mtima wanga.
2. Ndidzati kwa Mulungu, Musanditsutse;Mundidziwitse cifukwa ca kutsutsana nane.
3. Cikukomerani kodi kungosautsa,Kuti mupeputsa nchito yolemetsa manja anu,Ndi kuti muwalira pa uphungu wa oipa?
4. Muli nao maso a thupi kodi?Mupenya kodi monga umo apenyera munthu?
5. Masiku anu akunga masiku a munthu kodi,Zaka zanu zikunga masiku a munthu;
6. Kuti mufunsa mphulupulu yanga,Ndi kulondola coipa canga;
7. Cinkana mudziwa kuti sindiri woipa,Ndipo palibe wakupulumutsa m'dzanja lanu?
8. Manja anu anandiumba, nandiulunga monsemu,Koma mufuna kundiononga.
9. Mukumbukile kuti mwandiumba ngati dothi;Ndipo kodi mudzandibwezera kupfumbi?
10. Simunanditsanula kodi ngati mkaka,Ndi kundilimbitsa ngati mase?
11. Munandibveka khungu ndi mnofu,Ndi kundilumikiza mafupa ndi mitsempha,