Pamene pakupfuula iwe akupulumutse amene unawasonkhanitsa; koma mphepo idzawatenga, mpweya udzacotsa onse; koma iye amene andikhulupirira Ine adzakhala ndi dziko, nadzakhala naco colowa m'phiri langa lopatulika.