Tukula maso ako kuunguza-unguza, nuone; onsewa asonkhana pamodzi, nadza kwa iwe. Pali Ine, ati Yehova, iwe ndithu udzadzibveka wekha ndi iwo onse, monga ndi cokometsera, ndi kudzimangira nao m'cuuno ngati mkwatibwi.