Atero Yehova, Mombolo wanu, Woyera wa Israyeli: Cifukwa ca inu ndatumiza ku Babulo, ndipo ndidzatsitsira iwo onse monga othawa, ngakhale Akasidi m'ngalawa za kukondwa kwao.