Yehova adzaturuka ngati munthu wamphamvu; adzautsa nsanje ngati munthu wa nkhondo; Iye adzapfuula, inde adzakuwa zolimba; adzacita zamphamvu pa adani ace.