6. Taona, masiku afika, kuti zonse za m'nyumba mwako, ndi zimene atate ako anazikundika kufikira lero lino, zidzatengedwa kunka ku Babulo; sipadzatsala kanthu, ati Yehova.
7. Ndipo ana ako amene adzabadwa ndi iwe, amene udzabala, iwo adzawatenga, ndipo adzakhala adindo m'cinyumba cace ca mfumu ya ku Babulo.
8. Ndipo Hezekiya anati kwa Yesaya, Mau a Yehova, amene iwe wanena, ali abwino. Iye anatinso, Pakuti padzakhala mtendere ndi zoonadi masiku anga.