4. Ndipo iye anati, Kodi iwo anaona ciani m'nyumba mwanu? Ndipo Hezekiya anayankha, Zonse za m'nyumba mwanga iwo anaziona; palibe kanthu ka mwa cuma canga, kamene ine sindinawaonetse.
5. Ndipo Yesaya anati kwa Hezekiya, Imvani mau a Yehova wa makamu.
6. Taona, masiku afika, kuti zonse za m'nyumba mwako, ndi zimene atate ako anazikundika kufikira lero lino, zidzatengedwa kunka ku Babulo; sipadzatsala kanthu, ati Yehova.
7. Ndipo ana ako amene adzabadwa ndi iwe, amene udzabala, iwo adzawatenga, ndipo adzakhala adindo m'cinyumba cace ca mfumu ya ku Babulo.