Nenani kwa a mitima ya cinthenthe, Limbani, musaope; taonani, Mulungu wanu adza ndi kubwezera cilango, ndi mphotho ya Mulungu; Iye adzafika ndi kukupulumutsani.