Zingwe zako za ngalawa zamasulidwa; sizinathe kulimbitsa patsinde pa mlongoti wace, sizinathe kufutukula matanga; pamenepo ndipo colanda cacikulu, cofunkha cinagawanidwa; wopunduka nafumfula.