Iye amene ayenda molungama, nanena molunjika; iye amene anyoza phindu lonyenga, nasansa manja ace kusalandira zokometsera milandu, amene atseka makutu ace kusamva za mwazi, natsinzina maso ace kusayang'ana coipa;