6. Pakuti wopusa adzanena zopusa, ndi mtima wace udzacita mphulupulu, kucita zoipitsa, ndi kunena za Yehova molakwira, kusowetsa konse mtima wanjala, ndi kulepheretsa cakumwa ca waludzu.
7. Zipangizonso za womana ziri zoipa; iye apangira ziwembu zakuononga waumphawi ndi mau onama, ngakhale pamene wosowa alankhula zoona.
8. Koma mfulu aganizira zaufulu, nakhazikika m'zaufulu zomwe.
9. Ukani, akazi inu, amene mulinkukhala phe, mumve mau anga; mu ana akazi osasamalira, cherani makutu pa kulankhula kwanga.
10. Pakutha caka, kudza masiku ena inu mudzabvutidwa, inu akazi osasamalira; pakuti masika a mphesa adzasoweka, sadzatuta konse.