Cifukwa kuti Yerusalemu wapasulidwa, ndi Yuda wagwa; cifukwa kuti lilume lao ndi macitidwe ao akana Yehova, kuti autse mkwiyo wa m'maso a ulemerero wace.