5. Cifukwa Iye watsitsira pansi iwo amene anakhala pamwamba, mudzi wa pamsanje; Iye wautsitsa, wautsitsira pansi; waugwetsa pansi pa pfumbi.
6. Phazi lidzaupondereza pansi; ngakhale mapazi a aumphawi, ndi mapondedwe a osowa.
7. Njira ya wolungama iri njira yoongoka; Inu amene muli woongoka, mukonza njira ya wolungama.
8. Inde m'njira ya maweruziro anu, Yehova, ife talindira Inu; moyo wathu ukhumba dzina lanu, ndi cikumbukilo canu.
9. Ndi moyo wanga ndinakhumba Inu usiku; inde ndi mzimu wanga wa mwa ine ndidzafuna Inu mwakhama; pakuti pamene maweruziro anu ali pa dziko lapansi, okhala m'dziko lapansi adzaphunzira cilungamo.
10. Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira cilungamo; m'dziko la macitidwe oongoka, iye adzangocimwa, sadzaona cifumu ca Yehova.
11. Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona cangu canu ca kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamariza adani anu.
12. Yehova, udzatikhazikitsira mtendere; pakuti mwatigwirira nchito zathu zonse.