1. Tsiku limenelo adzayimba nyimbo imeneyi m'dziko la Yuda, Ife tiri ndi mudzi wolimba; Iye adzaikacipulumutso cikhale macemba ndi malinga.
2. Tsegulani pazipata, kuti mtundu wolungama, umene ucita zoonadi, ulowemo.
3. Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weni weni, cifukwa ukukhulupirirani Inu.