Iye ndithu adzakuzunguza, ndi kukuponyaponya ngati mpira m'dzido lalikuru; kumeneko iwe udzafa, ndipo kumeneko kudzakhala magareta a ulemerero wako, iwe wocititsa manyazi banja la mbuye wako.