Nthawi imeneyo Yehova ananena ndi Yesaya, mwana wa Amozi, nati, Muka numasule ciguduli m'cuuno mwako, nucicotse, nubvule nsapato yako ku phazi lako. Ndipo iye anatero, nayenda marisece, ndi wopanda nsapato,