Tsiku limenelo padzakhala midzi isanu m'dziko la Aigupto yolankhula cinenero ca Kanani, ndi yolumbira, Pali Yehova wa makamu; wina udzachedwa, Mudzi wa cionongeko.