Nditani nazo nsembe zanu zocurukazo? ati Yehova; ndakhuta nazo nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi mafuta a nyama zonenepa; sindisekera ndi mwazi wa ng'ombe zamphongo, ngakhale wa ana a nkhosa, ngakhale wa atonde.