Ndinachera khutu, ndinamva koma sananena bwino; panalibe munthu amene anatembenuka kusiya zoipa zace, ndi kuti, Ndacita ciani? yense anatembenukira njira yace, monga akavalo athamangira m'nkhondo.