Yehova Inu, maso anu sali pacoonadi kodi? munawapanda iwo, koma sanaphwetekedwa mtima; munawatha iwo, koma akana kudzudzulidwa; alimbitsa nkhope zao koposa mwala; akana kubwera.