16. Tsoka la Moabu layandikira kudza, nsautso yace ifulumiratu.
17. Inu nonse akumzungulira, mumcitire iye cisoni, inu nonse akudziwa dzina lace; muti, Cibonga colimba catyokatu, ndodo yokoma!
18. Iwe mwana wamkazi wokhala m'Diboni, utsike pa ulemerero wako, nukhale ndi ludzu; pakuti wakufunkha Moabu wakukwerera, iwe waononga malinga ako.
19. Iwe wokhala m'Aroeri, ima panjira, nusuzumire umfunse iye amene athawa, ndi mkazi amene apulumuka; nuti, Cacitidwa ciani?
20. Moabu wacitidwa manyazi, pakuti watyoka; kuwa nulire, nunene m'Arinoni, kuti Moabu wapasuka.
21. Ciweruzo cafika pa dziko lacidikha; pa Holoni, ndi pa Yaza, ndi pa Mefati;
22. ndi pa Diboni, ndi pa Nebo, ndi pa Beti-Dibilataimu;
23. ndi pa Kiriataimu, ndi pa Beti-Gamuli, ndi pa Beti-Meoni;