ndi kuti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Taonani Ine ndidzatuma ndidzatenga Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, mtumiki wanga, ndi kuika mpando wace wacifumu pa miyalayi ndaiyala; ndipo iye adzaibvundikira ndi hema wacifumu wace.