Pamenepo iwo anati kwa Yeremiya, Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika pakati pa ife, ngati siticita monga mwa mau onse Yehova Mulungu wanu adzakutumizani nao kwa ife.