Ndipo Yeremiya mneneri anati kwa iwo, Ndamva; taonani, ndidzapemphera kwa Yehova Mulungu wanu monga mwa mau anu; ndipo padzakhala kuti ciri conse Yehova adzakuyankhirani, ndidzakufotokozerani; sindidzakubisirani inu kanthu.