Ndipo mfumu anatuma Yehudi atenge mpukutuwo; ndipo anautenga kuturuka nao m'cipinda ca Elisama mlembi, Ndipo Yehudi anauwerenga m'makutu a mfumu, ndi m'makutu a akuru onse amene anaima pambali pa mfumu.