Atero Yehova, Ngati ukhoza kuyesa thambo la kumwamba, ndi kusanthula pansi maziko a dziko, pamenepo ndidzacotsa mbeu zonse za Israyeli cifukwa ca zonse anazicita, ati Yehova.